1 Kings 6:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chipata choloŵera ku chipinda chapansi chija chinali chakumwera kwa Nyumbayo. Anthu ankachita kukwera makwerero pochoka ku chipinda chapansi kupita ku chipinda chapakati, chimodzimodzi pochoka ku chipinda chapakati kupita ku chipinda chapamwamba.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kufikira ku zipinda za pakati, ndi kutuluka m'zapakatizo kulowa m'zachitatuzo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chipata cholowera ku chipinda chapansi chinali mbali ya kummwera kwa Nyumbayo. Panali makwerero okwerera ku chipinda chapakati ndiponso chipinda cha pamwamba.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Khomo lolowera m'zipinda za pakati linali ku mbali ya ku dzanja lamanja ya nyumba; ndipo anthu amakwerera pa makwerero ozunguniza, kutikira ku zipinda za pakati, ndi kuturuka m'zapakatizo kulowa m'zacitatuzo,