1 Kings 7:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Bwalo lalikulu kuzungulira nyumbayo lidamangidwa mizere itatu yamiyala yosemedwa, ndi mzere umodzi wa mitengo yamkungudza. Bwalo lam'kati la nyumbayo ndiponso khonde lake la nyumbayo adazimanga chimodzimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo bwalo lalikulu lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungudza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi chipinda cholowera cha nyumbayo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Bwalo lalikulu lozungulira nyumbayi linali ndi khoma la mizere itatu ya miyala yosemedwa ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza. Bwalo la mʼkati la Nyumba ya Yehova ndiponso khonde lake anazimanga mofanana.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo bwalo lalikuru lozingapo linali ndi mizere itatu ya miyala yosemasema, ndi mzere umodzi wa mitanda yamkungundza, monga bwalo la pakati pa nyumba ya Yehova, ndi likole la nyumbayo.