1 Kings 7:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali mwana wa mai wamasiye wa fuko la Nafutali, ndipo bambo wake anali wa ku Tiro, mmisiri wa mkuŵa. Huramuyo anali wanzeru kwambiri, womvetsa zinthu, ndiponso waluso popanga zinthu zilizonse zamkuŵa. Adafika kwa mfumu Solomoni, nagwira ntchito zonse za Solomoniyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iyeyo anali mwana wake wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali, atate wake anali munthu wa ku Tiro, mfundi wamkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira ntchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomoni namgwirira ntchito zake zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
mwana wa mkazi wamasiye wa fuko la Nafutali ndipo abambo ake anali a ku Turo, mʼmisiri wa mkuwa. Hiramu anali munthu wa luso lalikulu ndiponso wodziwa kupanga zinthu za mkuwa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomoni ndi kugwira ntchito zonse zimene anamupatsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iyeyo anali mwana wace wa mkazi wamasiye wa pfuko la Nafitali, atate wace anali munthu wa ku Turo, mfundi wa mkuwa; ndipo iye anadzala ndi nzeru ndi luntha ndi luso kugwira nchito zonse za mkuwa. Ndipo anadza kwa mfumu Solomo namgwirira nchito zace zonse.