1 Kings 7:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Huramu adasungunula mkuŵa, napanga nsanamira ziŵiri. Nsanamira ina msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu, ndipo mjintchi wake unali pafupi mamita asanu ndi theka. Nsanamirayo inali ndi mphako, ndipo kuchindikira kwake kunali ngati kuyesa zala zinai. Nsanamira inzakeyo inali chimodzimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wake wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo chingwe cha mikono khumi mphambu iwiri chinayesa thupi la nsanamira imodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anawumba nsanamira ziwiri za mkuwa, nsanamira iliyonse msinkhu wake unali mamita asanu ndi atatu ndipo thunthu lake akazunguliza chingwe, linali mamita asanu ndi theka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza iyeyu anaunda nsanamira ziwiri zamkuwa, msinkhu wace wa imodzi unali mikono khumi mphambu isanu ndi itatu; ndipo cingwe ca mikono khumi mphambu iwiri cinayesa thupi la nsanamira imodzi.