1 Kings 7:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adasungunula mkuŵa, napanganso mitu iŵiri, ndipo adaiika pamwamba pa nsanamira zija. Mutu wina kutalika kwake kunali mamita aŵiri nkanthu, ndipo winawo kutalika kwake kunalinso mamita aŵiri nkanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kuiika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wake wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzake mikono isanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanganso mitu iwiri ya mkuwa ndi kuyiika pamwamba pa nsanamira zija; mutu uliwonse unali wotalika kupitirirapo mamita awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga mitu iwiri ya mkuwa wosungunula, kulika pamwamba pa nsanamirazo, msinkhu wace wa mutu wina unali mikono isanu, ndi msinkhu wa mutu unzace mikono isanu.