1 Kings 7:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adapanganso mizere iŵiri ya zinthu zonga makangaza mozungulira pamwamba pa ukonde, kuti aphimbe mutu wa pamwamba pa nsanamira. Adachitanso chimodzimodzi ndi mutu winawo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nachita momwemo ndi mutu winawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anapanga mizere iwiri ya zinthu zonga makangadza mozungulira pamwamba pa maunyolo kukongoletsa mitu ya nsanamirazo. Anachita chimodzimodzi ndi mutu uliwonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'mwemo anapanga nsanamira, ndipo panali mizere iwiri yozungulira ukonde umodzi, kukuta ndi makangaza mituyi inali pamwambapo, nacita momwemo ndi mutu winawo.