1 Kings 7:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mitu imene inali pamwamba pa nsanamira m'khonde, inali itasemedwa ngati maluŵa a kakombo, kutalika kwake pafupifupi mamita aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa chipinda cholowera chinali ngati akakombo malembedwe ake, a mikono inai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitu imene inali pamwamba pa nsanamira mʼkhonde inali yooneka ngati maluwa okongola kwambiri. Kutalika kwake kunali pafupifupi mamita awiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mituyi inali pamwamba pa nsanamira za pa likole inali ngati akakombo malembedwe ace, a mikono inai.