1 Kings 7:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nyumbayo inali ndi chigawo china chachikulu chotchedwa Nyumba ya Nkhalango ya ku Lebanoni. M'litali mwake inali mamita 44, m'mimba mwake inali mamita 22, msinkhu wake unali mamita 13 ndi theka. Adaimanga pamwamba pa mizere inai ya nsanamira zamkungudza, ndipo panali mitanda yamkungudza pamwamba pa nsanamirazo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Anamanganso nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni, m'litali mwake munali mikono zana limodzi, kupingasa kwake mikono makumi asanu, ndi msinkhu wake mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anamanga nyumba yaufumu yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni yomwe mulitali mwake inali mamita 44, mulifupi mwake mamita 22, msinkhu wake mamita 13 ndi theka; ndipo inakhazikika pa mizere inayi ya mapanda a mkungudza yokhala ndi mitanda ya mkungudza yotanthalika pa mapandawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Anamanganso nyumba yochedwa Nkhalango ya Lebano, m'litali mwace munali mikono zana limodzi, kupingasa kwace mikono makumi asanu, ndi msinkhu wace mikono makumi atatu; naisanja pa mizere inai ya mapanda amkungudza, ndi mitanda yamkungudza yotanthalika mapandawo.