1 Kings 7:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mituyo inali pamwamba pa nsanamira ziŵiri zija, ndiponso pamwamba pa chigawo choulungika cha pambali pake pa ukondewo. Pa mutu umodzi panali makangaza okwanira 200 pa mizere iŵiri yozungulira, ndipo pa mutu winawo panalinso chimodzimodzi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwake mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga ndanda mutu winawo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa mitu yonse iwiri ya pamwamba pa nsanamira, pamwamba pa chigawo chonga mʼphika pafupi ndi cholukidwa ngati ukonde, panali makangadza 200 okhala mozungulira mʼmizere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panalinso mitu pamwamba pa nsanamira ziwirizo, pafupi pa mimbayo, inali m'mbali mwace mwa ukondewo; ndipo makangazawo anali mazana awiri, akukhala mizere yozinga nda nda mutu winawo.