1 Kings 7:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake Huramu adapanga thanki lamkuŵa. Thankilo linali loulungika. Pakamwa pake panali pa mamita anai ndi theka, kuyesa modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wa mamita aŵiri nkanthu ndipo kuzungulira m'thunthu mwake munali mamita 13 ndi theka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwake kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wake unali mikono isanu; ndi chingwe cha mikono makumi atatu chinalizungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka iye anapanga mbiya yayikulu yachitsulo. Inali yozungulira ndipo pakamwa pake panali pa mamita anayi ndi theka, poyeza modutsa pakati pake. Msinkhu wake unali wopitirirapo mamita awiri. Thunthu lake linali mamita 13.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayenganso thawale lamkuwa, kukamwa kwace kunali kwa mikono khumi, linali lozunguniza, ndi msinkhu wace unali mikono isanu; ndi cingwe ca mikono makumi atatu cinalizungulira.