1 Kings 7:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'munsi mwa milomo yake adazokotamo tizikho kuzunguliza thunthu lonse la thankilo, ndiye kuti dera lonse la mamita 13 ndi theka. Tizikhoto tinali m'mizere iŵiri, ndipo adaatipangira kumodzi ndi thankilo pamene ankalipanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'khosi mwake munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmunsi mwa mkombero wa mbiyayo anajambulamo tizikho kuzungulira thunthu lonse la mbiyayo, tizikho khumi pa theka la mita. Tizikhoto tinali mʼmizere iwiri ndipo anatipangira kumodzi ndi mbiyayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'khosi mwace munali ngati zikho zozinganiza m'mkono umodzi zikho khumi zakuzinganiza thawalelo; zikhozo zinayengedwa m'mizere iwiri poyengedwa thawalelo.