1 Kings 7:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adalisanjika pa ng'ombe zamkuŵa khumi ndi ziŵiri. Zitatu kuyang'ana kumpoto, zitatu kuyang'ana kuzambwe, zitatu kuyang'ana kumwera, zitatu kuvuma. Thankilo linali litakhazikika pa ng'ombezo, ndipo kuti miyendo yonse yamunsi ya ng'ombezo idaaloza cham'kati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Linasanjikika pa ng'ombe khumi mphambu ziwiri, zitatu zinapenya kumpoto, zitatu kumadzulo, zitatu kumwera, zitatu kum'mawa; ndipo thawalelo linakhazikika pamwamba pa izo; ndipo nkholo zao zinayang'anana.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbiyayo anayisanjika pa ngʼombe zamkuwa khumi ndi ziwiri, zitatu zoyangʼana kumpoto, zitatu zoyangʼana kumadzulo, zitatu zoyangʼana kummwera ndipo zitatu zoyangʼana kummawa. Mbiyayo inakhazikika pamwamba pa ngʼombezo, ndipo miyendo yake yonse yakumbuyo ya ngʼombezo inkaloza mʼkati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika