1 Kings 7:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Thankilo kuchindikira kwake kunali ngati chikhatho. M'milomo mwake munkaoneka ngati m'milomo mwa chikho, ngati duŵa la kakombo. Munkaloŵa madzi okwanira malita 40,000.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kuchindikira kwake kunali ngati chikhato cha munthu, ndipo mlomo wake unasadamuka ngati mlomo wa chomwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikulu zikwi ziwiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbiyayo inali yonenepa ngati chikhatho ndipo mkombero wake unali ngati mkombero wa chikho, ngati duwa lokongola kwambiri. Mʼmbiyamo munkalowa madzi okwana malita 40,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kucindikira kwace kunali ngati m'manja mwa munthu, ndipo mlomo wace unasadamuka ngati mlomo wa comwera, ngati maluwa akakombo, analowamo madzi a mitsuko yaikuru zikwi ziwiri.