1 Kings 7:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono adapanganso maphaka khumi amkuŵa oyenda. Phaka lililonse muutali mwake linali pafupifupi mamita aŵiri, muufupi mwake linalinso pafupifupi mamita aŵiri, ndipo msinkhu wake unali mita imodzi nkanthu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwake mwa phaka limodzi mikono inai, ndi msinkhu wake mikono itatu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapanganso maphaka khumi a mkuwa. Phaka lililonse mulitali mwake linali pafupifupi mamita awiri, mulifupi mwake linali pafupifupi mamita awiri, ndipo msinkhu wake unali kupitirirapo mita imodzi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga maphaka khumi amkuwa, m'litali mwace mwa phaka limodzi mikono inai, ndi kupingasa kwace mikono inai, ndi msinkhu wace mikono itatu.