1 Kings 7:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo pa matabwawo panali zithunzi za mikango, ng'ombe zamphongo ndi akerubi. Tsono pa mafuremuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ng'ombe zamphongozo, adazokotapo nkhata zamaluŵa mopendeketsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pa matsekezerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali chosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakati pa matabwa a mʼmbali ndi maferemu panali zithunzi za mikango, ngʼombe zazimuna ndi akerubi. Pa maferemuwo, pamwamba ndi pansi pake pa mikangoyo ndi ngʼombe zazimunazo anajambulapo nkhata za maluwa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pa matsekerezo a pakati pa mbano panali ngati mikango ndi ng'ombe ndi akerubi, ndi pamwamba pa mbano panali cosanjikirapo; ndipo pansi pa mikango ndi ng'ombe panaphatikizika zotsetseremba zoyangayanga zokoloweka.