1 Kings 7:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuwonjezera apo, phaka lililonse linali ndi mikombero inai yamkuŵa ndiponso mitanda yake yamkuŵanso. Ndipo pa ngodya zake zinai panali zogwiriziza mbale zosambira. Popanga zogwiriziza mbalezo, m'mbali mwake adalochamo ndi nkhata zamaluŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo phaka lililonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngodya zake zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Phaka lililonse linali ndi mikombero ya mkuwa inayi ndi mitandanso ya mkuwa, ndipo phaka lililonse linali ndi zogwiriziza mbale zosambira pa ngodya zake zinayi, zopangidwa limodzi ndi nkhata za maluwa mbali zake zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo phaka lid lonse linali ndi njinga zamkuwa zinai ndi mitanda yamkuwa, ndipo ngondya zace zinai zinali ndi mapewa; pansi pa thawale panali mapewa oyengeka pa mbali pa zophatikizika zonse.