1 Kings 7:31 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kukamwa kwake kunali kozungulira ndipo kudabzola pamwamba pa phakalo masentimita 44. Kuzama kwake kunali masentimita 18. Pakamwapo panali zozokota zokometsera. Ndipo matabwa ake anali aphanthiphanthi a mbali zofanana, osati oulungika ai.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakamwa pake m'katimo pamwamba pa chosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pake panali posadamuka, monga mapangidwe ake a chosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pake panali zolemba ndi matsekerezo ake anali aphwamphwa, si ozunguniza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼkati mwa phakalo munali malo otsekuka amene anali ndi feremu yozungulira ndipo anali ozama theka la mita. Malo otsekukawa anali wozungulira, ndipo pamodzi ndi tsinde lake anali otalika masentimita 44. Kuzungulira pa malo otsekukawa panajambulidwa zokometsera. Matabwa oyimikira phakali anali ofanana mbali zonse, osati ozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakamwa pace m'katimo pamwamba pa cosanjikira, panayesa mkono umodzi; koma pakamwa pace panali posadamuka, monga mapangidwe ace a cosanjikira, mkono umodzi ndi nusu; ndiponso pakamwa pace panali zolemba ndi matsekerezo ace anali amphwamphwa, si ozunguniza.