1 Kings 7:36 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamwamba pa zogwiriziza zakezo ndi matabwa akewo panali zithunzi za akerubi, mikango ndiponso mitengo ya mgwalangwa, malinga ndi m'mene unaliri mpata wokwanira chilichonse. Pozungulira adalocha ndi nkhata zamaluŵa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mapanthi mwa mbano zake ndi pa matsekerezo ake analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ake a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Paliponse pamene panali malo woti nʼkujambulapo, pa zogwiriziza ndi pa matabwa, anagobapo zithunzi za akerubi, mikango ndi mitengo ya mgwalangwa. Anajambulanso nkhata za maluwa mozungulira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mapanthi mwa mbano zace ndi pa matsekerezo ace analemba ngati akerubi ndi mikango ndi migwalangwa, monga mwa malo ace a zonsezo, ndi zoyangayanga zozungulira.