1 Kings 7:38 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambuyo pake adapanga mbiya zikuluzikulu khumi zamkuŵa. M'mbiya iliyonse munkaloŵa madzi a malita 800, ndipo pakamwa pake panali pafupifupi mamita aŵiri, kuyesa modutsa. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi mbiya yake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anapanga mbiya zaphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikulu makumi anai, ndipo mbiya iliyonse inali ya mikono inai: pa phaka lililonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka anapanga mabeseni akuluakulu khumi a mkuwa; beseni lililonse munkalowa madzi a malita 800, ndipo poyeza modutsa, pakamwa pake panali pafupifupi mamita awiri. Maphaka khumi aja, lililonse linali ndi beseni lake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anapanga mbiya zamphwamphwa khumi zamkuwa; m'mbiya imodziyo munalowamo madzi a mitsuko yaikuru makumi anai, ndipo mbiya iri yonse inali ya mikono inai: pa phaka liri lonse la maphaka aja khumi panakhala mbiya imodzi.