1 Kings 7:42 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adatsirizanso kupanga makangaza 400 a maukonde aŵiri aja, mizere iŵiri ya makangaza pa ukonde uliwonse, kuphimbira ziwaya ziŵiri zija za kunsonga kwa makapotolosi okhala pamwamba pa nsanamira zija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
makangadza 400 a maukonde awiri okongoletserawo (mizere iwiri ya makangadza pa ukonde uliwonse, kukongoletsa mbale za mitu yapamwamba pa nsanamira);
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi makangaza mazana anai a maukonde awiriwo, mizere iwiri ya makangaza a ukonde umodzi kuphimbira mbale ziwiri za mitu inali pa nsanamirazo,