1 Kings 7:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Solomoni adangozisiya ziŵiya zimenezo osaziyesa pa sikelo, chifukwa zidaalipo zambirimbiri. Motero kulemera kwa mkuŵawo sikudadziŵike.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinachuluka ndithu; kulemera kwake kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni sanayeze ziwiya zonsezi chifukwa zinali zambiri ndipo kulemera kwa mkuwa sikunadziwike.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anazileka zipangizo zonse osaziyesa, popeza zinacuruka ndithu; kulemera kwace kwa mkuwa wonsewo sikunayeseka.