1 Kings 7:49 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
zoikaponyale za golide weniweni, kumwera zisanu, kumpoto zisanu, m'kati mwenimweni mwa malo opatulika. Adapangitsa maluŵa, nyale ndi mbano, zonse zagolide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi zoikapo nyali za golide woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, chakuno cha chipinda chamkati, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolide;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
zoyikapo nyale zagolide weniweni (dzanja lamanja zisanu ndipo zisanu zina ku dzanja lamanzere, mʼkati mwenimweni mwa malo opatulika); maluwa agolide, nyale ndi mbaniro;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi zoikapo nyali za golidi woyengetsa, zisanu ku dzanja lamanja, zisanu kulamanzere, cakuno ca monenera, ndi maluwa ndi nyali ndi mbano zagolidi;