1 Kings 7:51 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero Mfumu Solomoni adatsiriza ntchito zonse za ku Nyumba ya Chauta. Tsono adabwera ndi zinthu zonse zimene Davide bambo wake adaazipereka, siliva, golide, ndi ziŵiya. Adaziika m'zipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Motero ntchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomoni anachitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomoni analonga zinthu adazipatula Davide atate wake, ndizo siliva ndi golide ndi zipangizo zomwe naziika mosungira chuma cha nyumba ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene ntchito yonse imene Mfumu Solomoni inagwira pa Nyumba ya Yehova inatha, anabwera ndi zinthu zonse zimene abambo ake Davide anazipereka: siliva, golide ndi ziwiya. Anaziyika mʼzipinda zosungiramo chuma cha ku Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Motero nchito zonse zinatsirizika, zimene mfumu Solomo anacitira nyumba ya Yehova. Ndipo Solomo analonga zinthu adazipatula Davide atate wace, ndizo siliva ndi golidi ndi zipangizo zomwe naziika mosungira cuma ca nyumba ya Yehova.