1 Kings 7:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Panali chigawo chinanso chachikulu chotchedwa Holo ya Nsanamira. M'litali mwake inali ya mamita 22, m'mimba mwake inali ya mamita 13 ndi hafu. Patsogolo pake panali kakhonde ka nsanamira kokhala ndi denga lake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anamanga khonde la nsanamira, m'litali mwake munali mikono makumi asanu, kupingasa kwake mikono makumi atatu; ndipo panali khonde lina patsogolo pake, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pakepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anapanga Chipinda cha Nsanamira. Mulitali mwake munali mamita 22, mulifupi mwake munali mamita 13 ndi theka. Patsogolo pake panali khonde ndi nsanamira zokhala ndi denga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anamanga khumbi la nsanamira, m'litali mwace munali mikono makumi asanu, kupingasa kwace mikono makumi atatu; ndipo panali khumbi lina patsogolo pace, ndi nsanamira ndi mitanda patsogolo pacepo.