1 Kings 7:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono nyumba yakeyake kumene ankayenera kukakhalako, adaimanga ku bwalo lina, kumbuyo kwa holo imeneyo. Adaimanga chimodzimodzi ngati holoyo. Ndipo adamanganso chigawo china chofanana ndi holo ya Mpando wachifumu ija kumangira mkazi wake, mwana wa Farao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nyumba yake yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khondelo, linamangidwa chimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomoni, yofanafana ndi khonde limeneli.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo nyumba yake yodzakhalamo anayimanga kumbuyo kwa chipindacho. Nyumbayo anayimanga mofanana ndi Chipindacho. Solomoni anamanga nyumba inanso yofanana ndi chipindachi, kumangira mkazi wake mwana wa Farao.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nyumba yace yakukhalamo iye, m'bwalo lina la m'tsogolo mwa khumbilo, linamangidwa cimodzimodzi. Anammangiranso nyumba mwana wamkazi wa Farao, amene adamkwatira Solomo, yofanafana ndi khumbi limeneli.