1 Kings 7:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zonsezi zidamangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene adaisema potsata miyeso yake yofunika, yochekedwa ndi sowo m'kati ndi kunja komwe. Miyala yotere adamangira nyumba kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, kuyambiranso m'bwalo la Nyumba ya Chauta mpaka ku bwalo lalikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, malingana ndi miyeso yake, yocheka ndi mipeni ya manomano m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumaziko kufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikulu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nyumba zonsezi, kuyambira kunja mpaka ku bwalo lalikulu ndiponso kuchokera pa maziko mpaka pamwamba pa khoma, zinapangidwa ndi miyala yabwino kwambiri imene anayisema potengera miyeso yake yoyenera ndipo anayisalaza ndi macheka mʼkati ndi kunja komwe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Izi zonse zinali za miyala ya mtengo wapatali yosemasema, ya muyeso muyeso, yoceka ndi mipeni ya mano mana m'katimo ndi kunjako, kuyambira kumazikokufikira kumutu, momwemonso kunjako ku bwalo lalikuru,