1 Kings 8:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja adaati, ‘Kuyambira tsiku limene ndidatulutsa anthu anga Aisraele ku Ejipito, sindidasankhepo mzinda pakati pa mafuko onse a Aisraele woti anthu amangeko nyumba m'mene dzina langa lizimvekamo. Koma ndidasankha Davide kuti azilamulira anthu anga Aisraele.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Kuyambira tsiku lakutulutsa Ine anthu anga Aisraele m'dziko la Ejipito, sindinasankha mudzi uliwonse mwa mafuko onse a Israele kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisraele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
‘Kuyambira tsiku limene ndinatulutsa anthu anga Aisraeli ku Igupto, sindinasankhe mzinda wina uliwonse pa fuko lina lililonse la Aisraeli kuti kumeneko andimangire Nyumba, koma ndasankha Davide kuti alamulire anthu anga Aisraeli.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Kuyambira tsiku lakuturutsa Ine anthu anga Aisrayeli m'dziko la Aigupto, sindinasankha mudzi uli wonse mwa mafuko onse a Israyeli kumangamo nyumba yokhalamo dzina langa, koma ndinasankha Davide kukhala mfumu ya anthu anga Aisrayeli.