1 Kings 8:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono, Inu Chauta, Mulungu wa Aisraele, mukumbukire zimene zija mudalonjeza Davide bambo wanga, mtumiki wanu, pamene mudati, ‘Sipadzasoŵa munthu pa banja lako wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa dziko la Israele, malinga ana ako akamasamala mkhalidwe wao, ndi kumayenda pamaso panga anga monga momwe iweyo wayendera pamaso panga.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israele, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga chimene chija mudamlonjezacho, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wachifumu wa Israele; komatu ana ako achenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ndipo tsopano, Inu Yehova Mulungu wa Israeli, sungani zimene munalonjeza kwa abambo anga Davide, mtumiki wanu, pamene munati, ‘Sudzasowa munthu wokhala pamaso panga pa mpando waufumu wa Israeli, ngati ana ako adzasamalira mayendedwe awo mokhulupirika monga iwe wachitira.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsopano, Yehova Mulungu wa Israyeli, msungireni mtumiki wanu Davide atate wanga cimene cija mudamlonjezaco, ndi kuti, Sadzakusowa munthu pamaso panga wokhala pa mpando wacifumu wa Israyeli; komatu ana ako acenjere njira yao, kuti akayende pamaso panga monga umo unayendera iwe pamaso panga.