1 Kings 8:30 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Imvani pemphero lopemba la mtumiki wanu ndiponso la anthu anu Aisraele, pamene akupemphera ku malo ano. Ndithu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mukamva, mukhululuke.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisraele, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Imvani pembedzero la mtumiki wanu ndi la anthu anu Aisraeli pamene akupemphera akuyangʼana malo ano. Imvani kumwambako, malo anu amene mumakhala; ndipo mukamva muzitikhululukira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mverani pembedzero la kapolo wanu ndi la anthu anu Aisrayeli, pamene adzapemphera molunjika kumalo kuno; ndipo mverani Inu m'Mwamba mokhala Inumo; ndipo pamene mukumva, khululukirani.