1 Kings 8:33 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Anthu anu Aisraele atagonjetsedwa ndi adani ao chifukwa chakuti adakuchimwirani, pambuyo pake nkubwerera kwa Inu ndi kutamanda dzina lanu, napemphera ndi kupemba kwa Inu m'Nyumba muno,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu anu Aisraele akawakantha adani ao chifukwa cha kuchimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, ndi kuvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu anu Aisraeli akagonja kwa adani awo chifukwa akuchimwirani, ndipo akatembenukira kwa Inu ndi kuvomereza Dzina lanu, kupemphera ndi kupembedzera kwa Inu mʼNyumba ino,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu anu Aisrayeli akawakantha adani ao cifukwa ca kucimwira Inu, ndipo akabweranso kwa Inu, lodi kubvomereza dzina lanu, ndi kupemphera, ndi kupembedza Inu m'nyumba muno;