1 Kings 8:34 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inuyo mumve kumwambako, ndipo mukhululukire tchimo la anthu anu Aisraele, kenaka muŵabwezenso ku dziko limene Inu mudapatsa makolo ao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraele, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako ndi kukhululukira tchimo la anthu anu Aisraeli ndi kuwabweretsa ku dziko limene munawapatsa makolo awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mverani Inu m'Mwambamo, ndi kukhululukira cimo la anthu anu Aisrayeli, ndi kuwabwezera ku dziko limene munapatsa makolo ao.