1 Kings 8:36 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
pamenepo Inuyo mumve kumwambako, mukhululukire tchimo la atumiki anu, anthu anu Aisraele. Inu muziŵaphunzitsa njira yabwino yoti aziyendamo, ndipo muzigwetsa mvula pa dziko lanu limene mudapatsa anthu anu kuti likhale choloŵa chao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira tchimo la akapolo anu, ndi la anthu anu Aisraele; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako ndipo muwakhululukire atumiki anu, anthu anu Aisraeli. Aphunzitseni makhalidwe oyenera ndipo gwetsani mvula mʼdziko limene munapereka kwa anthu anu monga cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
pamenepo mverani Inu m'Mwamba, ndi kukhululukira cimo la akapolo anu, ndi la, anthu anu Aisrayeli; pakuti muwaphunzitsa njira yokoma ayenera kuyendamo, ndi kupatsa mvula pa: dziko lanu, limene munawapatsa anthu anu likhale colowa cao.