1 Kings 8:37 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwina mwake m'dzikomo mudzaloŵa njala, mliri, dzimbiri lapambeu kapena chinoni, dzombe kapena kapuchi. Mwina adani ao adzaŵazinga ku mzinda wao wina uliwonse. Mwina padzakhala mliri wa mtundu wina, kapena matenda a mtundu uliwonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'dziko mukakhala njala, mukakhala mliri, mlaza, chinoni, dzombe, kapena kapuchi, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uliwonse, kapena nthenda;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene mʼdziko mwagwa njala kapena mliri, chinoni kapena chiwawu, dzombe kapena kapuchi, kapena pamene mdani wazungulira mzinda wawo wina uliwonse, kaya mavuto kapena matenda abwera,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'dziko mukakhala odala, mukakhala mliri, mlaza, cinoni, dzombe, kapena kapuci, adani ao akawamangira misasa m'dziko la midzi yao, mukakhala mliri uti wonse, kapena nthenda;