1 Kings 8:43 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu mumve kumwambako kumene mumakhala, ndipo mumchitire mlendoyo zonse zimene wakupemphani. Muchite zimenezi kuti anthu a mitundu yonse ya pa dziko lapansi adziŵe dzina lanu ndipo azikumverani, monga m'mene amachitira Aisraele anthu anu, ndipo adziŵe kuti Nyumba imene ndaimangayi imadziŵika ndi dzina lanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisraele, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yatchedwa dzina lanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
pamenepo imvani kumwambako, malo anu okhalamo, ndipo muchite zonse zimene mlendoyo akukupemphani, kotero kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu ndi kukuopani monga amachitira anthu anu Aisraeli, ndipo adziwe kuti Nyumba ino imene ndakumangirani imadziwika ndi Dzina lanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
mverani Inu m'Mwamba mokhala Inu, ndipo citani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa Inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziwe dzina lanu, kuopa Inu, monga amatero anthu anu Aisrayeli, ndi kuti adziwe kuti nyumba yino ndaimangayi yachedwa dzina lanu.