1 Kings 8:46 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mwina Aisraelewo adzakuchimwirani, poti palibe munthu amene sachimwa, ndiye Inuyo nkudzaŵakwiyira ndi kuŵapereka kwa adani, kuti aŵatenge ukapolo kupita nawo ku dziko lakutali kapena lakufupi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akachimwira Inu, popeza palibe munthu wosachimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kunka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pamene akuchimwirani, popeza palibe munthu amene sachimwa, ndipo Inu nʼkuwakwiyira ndi kuwapereka kwa mdani, amene adzawatenga ukapolo kupita ku dziko lake, kutali kapena pafupi;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akacimwira Inu, popeza palibe munthu wosacimwa, ndipo mukakwiya nao ndi kuwapereka kwa adani, kuti iwo awatenge ndende kumka nao ku dziko la adani, ngati kutali kapena kufupi,