1 Kings 8:47 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono, ali akapolo kuchilendoko, akazindikira kuchimwa kwao natembenuka mtima ndi kupemphera kwa Inu modzichepetsa m'dziko la anthu amene adaŵagwira ukapolowo, nkumanena kuti, ‘Tachimwa, tachita zosayenera, tapalamula ndithu’.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo akakumbukira mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza Inu m'dziko iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tachimwa, ndipo tachita mphulupulu, tachita moipa;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ngati asintha maganizo ali ku dziko la ukapololo ndi kulapa ndi kukudandaulirani mʼdziko la owagonjetsa ndi kunena kuti, ‘Ife tachimwa, tachita zolakwa, tachita zinthu zoyipa,’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo akakumbukila mitima yao, ali kudziko kumene anatengedwa ukapolo, nakalapa, nakapembedza inu m'dziko la iwo anawatenga ndende, ndi kuti, Tacimwa, ndipo tacita mphulupulu, tacita moipa;