1 Kings 8:48 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthuwo akabwerera kwa Inu ndi nzeru zao zonse ndi mtima wao wonse, m'dziko la adani ao kumene adaŵatengera ukapolo, ndipo akapemphera kwa Inu choyang'ana ku dziko lao limene Inu mudapatsa makolo ao, ku mzinda umene Inu mudausankha ndiponso ku Nyumba imene ine ndakumangiraniyi yomveketsa dzina lanu,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, kumudzi munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo ngati abwerera kwa Inu ndi mtima wawo wonse ndi moyo wawo wonse mʼdziko la adani awo amene anawatenga ukapolo, ndi kupemphera kwa Inu moyangʼana dziko limene munapereka kwa makolo awo, moyangʼana mzinda umene munawusankha ndiponso Nyumba imene ine ndamangira Dzina lanu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo akabwerera kwa Inu ndi mtima wao wonse ndi moyo wao wonse, m'dziko la adani ao adawatenga ndendewo, ndipo akapemphera kwa Inu molunjika ku dziko lao munapatsa makolo aolo, ku mudzi munausankha Inu, ndi kunyumba ndamangira dzina lanu;