1 Kings 8:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumu Solomoni pamodzi ndi gulu lonse la Aisraele amene adaasonkhana pamaso pake, ataima patsogolo pa Bokosi lachipanganolo, ankapereka nsembe za nkhosa ndi ng'ombe zosaŵerengeka.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Solomoni ndi msonkhano wonse wa Israele wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, chifukwa cha unyinji wao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
ndipo Mfumu Solomoni ndi gulu lonse la Aisraeli amene anasonkhana naye anali patsogolo pa Bokosi la Chipangano, akupereka nsembe nkhosa zambiri ndi ngʼombe zambiri zosawerengeka.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Israyeli wosonkhana kwa iye anali naye kulikasa, naphera nkhosa ndi ng'ombe za nsembe zosawerengeka ndi zosadziwika, cifukwa ca unyinji wao.