1 Kings 8:50 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono muŵakhululukire anthu anu okuchimwiraniwo, mukhululukire machimo ao onse okupandukirani. Ndipo mufeŵetse mitima ya anthu amene adaŵagwira ukapolo aja, kuti nawonso aŵachitire chifundo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kukhululukira anthu anu adachimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adapalamula nazo kwa Inu; ndipo muwachititsire chifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awachitire chifundo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo khululukirani anthu anu amene akuchimwirani. Khululukirani zolakwa zonse akuchitirani ndipo mufewetse mitima ya amene anawagonjetsawo kuti awachitire chifundo;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi kukhululukira anthu anu adacimwira Inu ndi mphulupulu zao zonse adaparamula nazo kwa Inu; ndipo muwacititsire cifundo iwo amene anawagwira ndende, kuti awacitire cifundo;