1 Kings 8:53 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pakuti Inu mudaŵasiyanitsa ndi anthu onse a pa dziko lapansi, kuti akhale anthu anuanu, monga momwe Inu mudanenera kudzera mwa Mose mtumiki wanu, pamene munkatulutsa makolo athu ku Ejipito, Inu Chauta Mulungu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale cholowa chanu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munatulutsa makolo athu m'Ejipito, Yehova Mulungu Inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti Inu munawasiyanitsa ndi anthu a mitundu ina yonse ya dziko lonse kuti akhale cholowa chanu, monga momwe munanenera kudzera mwa mtumiki wanu Mose pamene Inu, Ambuye Yehova, munatulutsa makolo athu ku Igupto.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Popeza Inu munawapatula pa anthu onse a pa dziko lapansi akhale colowa canu, monga munanena ndi dzanja la Mose mtumiki wanu, pamene munaturutsa makolo athu m'Aigupto, Yehova Mulungu Inu.