1 Kings 8:56 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Atamandike Chauta amene adaŵapatsa mtendere anthu ake Aisraele potsata zimene adaalonjeza. Palibe mau ndi amodzi omwe amene adapita pachabe pa zinthu zonse zabwino zimene adaalonjeza, polankhula kudzera mwa Mose mtumiki wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ake Aisraele, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayike mau amodzi a mau ake onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Atamandike Yehova, amene wapereka mpumulo kwa anthu ake Aisraeli monga momwe analonjezera. Palibe mawu ndi amodzi omwe amene anapita pachabe pa malonjezo ake onse abwino amene anawapereka kudzera mwa mtumiki wake Mose.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Wolemekezeka ndi Yehova amene anapumulitsa anthu ace Aisrayeli, monga mwa zonse analonjezazo; sanatayika mau amodzi a mau ace onse abwino, amene analankhula ndi dzanja la Mose mtumiki wace.