1 Kings 8:59 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mau angaŵa amene ndanena mopemba pamaso pa Chauta, Mulungu wathu, asaŵaiŵale mauwo masana ndi usiku. Chauta Mulungu wathu alimbikitse mtumiki wakene ndiponso athandize Aisraele anthu ake, poŵapatsa zosoŵa zao zatsikunditsiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wake, ndi mlandu wa anthu ake Aisraele, mlandu wa tsiku pa tsiku lake;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo mawu angawa, amene ndapemphera pamaso pa Yehova, asayiwalike pamaso pa Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, ndipo Iye alimbikitse mtumiki wake ndiponso athandize Aisraeli, anthu ake powapatsa zosowa zawo za tsiku ndi tsiku,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mau anga amenewa ndapembedzera nao pamaso pa Yehova akhale pafupi ndi Yehova Mulungu wathu usana ndi usiku, kuti alimbitse mlandu wa kapolo wace, ndi mlandu wa anthu ace Aisrayeli, mlandu wa tsiku pa tsiku lace;