1 Kings 8:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ansembe adafika nalo ndi Bokosi lachipangano la Chauta ku malo ake a m'kati mwenimweni mwa Nyumbayo, ku malo opatulika kopambana, naliika kunsi kwa mapiko a akerubi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ansembe analonga likasa la chipangano cha Yehova kumalo kwake, ku chipinda chamkati, ku malo opatulika kwambiri, munsi mwa mapiko a akerubi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ansembe anafika nalo Bokosi la Chipangano la Yehova mʼchipinda chamʼkati mwenimweni, Malo Opatulika Kwambiri, ndipo analiyika pansi pa mapiko a akerubi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ansembe analonga likasa la cipangano ca Yehova kumalo kwace, ku monenera mwa nyumba, ku malo opatulikitsa, munsi mwa mapiko a akerubi,