1 Kings 8:63 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Solomoni adapereka nsembe zachiyanjano kwa Chauta pakupha ng'ombe 22,000 ndi nkhosa 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraele onsewo adaipereka Nyumba ya Chauta ija.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Solomoni anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israele onse anapereka nyumbayo ya Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Solomoni anapereka nsembe zachiyanjano kwa Yehova: ngʼombe 22,000, nkhosa ndi mbuzi 120,000. Motero mfumu pamodzi ndi Aisraeli onse anapatula Nyumba ya Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Solomo anaphera nsembe yamtendere, yophera kwa Yehova ng'ombe zikwi makumi awiri mphambu ziwiri, ndi nkhosa zikwi zana limodzi mphambu makumi awiri. Momwemo mfumu ndi ana a Israyeli onse anapereka nyumbayo ya Yehova.