1 Kings 8:64 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku lomwelo mfumuyo idapatulanso malo am'kati a bwalo limene linali kumaso kwa Nyumba ya Chauta. Paja kumeneko nkumene adaperekerako nsembe yopsereza, ndiponso chopereka cha chakudya, kudzanso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano zija. Adaachita izi chifukwa choti guwa lamkuŵa limene linali m'malo opatulika a Chauta linali lochepa kwambiri, kotero kuti sikudatheke kuperekerapo nsembe zonse zopsereza ndi zaufa ndiponso nthuli zamafuta za nsembe zachiyanjano.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pake pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidachepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku lomwelo mfumu inapatulanso malo a pakati pa bwalo limene linali kutsogolo kwa Nyumba ya Yehova ndiponso nthuli za mafuta za nsembe yachiyanjano, chifukwa guwa lansembe la mkuwa limene linali pamaso pa Yehova linali lochepa kwambiri ndipo nsembe zonse zopsereza, nsembe zachakudya, ndi nthuli za mafuta a nsembe zachiyanjano sizikanakwanirapo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lomwelo mfumu inapatulira Mulungu pakati pace pa bwalo la ku khomo la nyumba ya Yehova; pakuti pomwepo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe yaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere; popeza guwa la nsembe lamkuwa linali pamaso pa Yehova lidacepa kulandira nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi mafuta a nsembe zamtendere.