1 Kings 8:65 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho nthaŵi imeneyo Solomoni adachita chikondwerero, pamodzi ndi Aisraele onse. Unali msonkhano waukulu kwambiri, kuyambira ku chipata cha Hamati mpaka ku kamtsinje ka Ejipito. Adachita chikondwerero chimenechi chopembedza Chauta Mulungu wathu, masiku asanu ndi aŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nthawi yomweyo Solomoni anachita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israele yense pamodzi naye, msonkhano waukulu wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Ejipito, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Choncho nthawi imeneyi, Solomoni anachita chikondwerero pamodzi ndi Aisraeli onse. Unali msonkhano waukulu, kuyambira ku Lebo Hamati mpaka ku Chigwa cha ku Igupto. Anachita chikondwerero chimenechi pamaso pa Yehova Mulungu wathu kwa masiku asanu ndi awiri, anawonjezerapo masiku ena asanu ndi awiri, onse pamodzi ngati masiku 14.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nthawi yomweyo Solomo anacita madyerero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndi Israyeli yense pamodzi naye, msonkhano waukuru wakuyambira polowera ku Hamati kufikira ku nyanja ya ku Aigupto, masiku asanu ndi awiri, ndi masiku asanu ndi awiri ena, ndiwo masiku khumi mphambu anai.