1 Kings 8:66 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu, Solomoni adauza anthuwo kuti azipita. Pompo anthuwo adathokoza mfumuyo, ndipo adapita kwao ndi mtima wokondwa ndi wosangalala, chifukwa cha zokoma zonse zimene Chauta adaachitira Davide mtumiki wake, ndi anthu ake Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku lachisanu ndi chitatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima chifukwa cha zokoma zonse Yehova anachitira Davide mtumiki wake, ndi Israele anthu ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku lachisanu ndi chitatu Solomoni anawuza anthu kuti apite kwawo. Anthuwo anathokoza mfumu ndipo kenaka anapita kwawo mokondwa ndi mosangalala mʼmitima mwawo chifukwa cha zinthu zabwino zimene Yehova anachitira mtumiki wake Davide ndi anthu ake Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku lacisanu ndi citatu anawauza anthu apite; ndipo iwo anadalitsa mfumu, napita ku mahema ao osekera ndi okondwera mtima cifukwa ca zokoma zonse Yehova anacitira Davide mtumiki wace, ndi Israyeli anthu ace.