1 Kings 8:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
M'Bokosimo munalibe kanthu kena kalikonse, kupatula miyala iŵiri yokha ija imene Mose adaaikamo ku Horebu, kumene Chauta adaachita chipangano ndi Aisraele, iwowo atatuluka ku dziko la Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja a mwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israele, potuluka iwo m'dziko la Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼbokosimo munalibe kanthu kena kalikonse kupatula miyala iwiri imene Mose anayikamo ku Horebu, kumene Yehova anachita pangano ndi Aisraeli atatuluka mʼdziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munalibe kanthu m'likasamo koma magome awiri aja amwala Mose anawalongamo pa Horebu, pamene Yehova anapangana ndi ana a Israyeli, poturuka iwo m'dziko la Aigupto.