1 Kings 9:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Hiramu wa ku Tiro ndiye ankapereka kwa Solomoni mitengo ya mkungudza, ya paini, ndiponso golide monga m'mene Solomoni ankazifunira. Ndipo mfumu Solomoni adapatsa Hiramu mizinda makumi aŵiri ya m'dziko la Galilea.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
popeza Hiramu mfumu ya Tiro adamthandiza Solomoni ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golide yemwe, monga momwe iye anafuniramo, chifukwa chake mfumu Solomoni anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Solomoni anapereka mizinda makumi awiri ya ku Galileya kwa Hiramu mfumu ya ku Turo chifukwa Hiramu nʼkuti atapereka mitengo yonse ya mkungudza ndi ya payini ndiponso golide yense zimene Solomoni ankazifuna.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
popeza Hiramu mfumu ya Turo adamthandiza Solomo ndi mitengo yamkungudza ndi yamlombwa ndi golidi yemwe, monga momwe iye anafuniramo, cifukwa cace mfumu Solomo anampatsa Hiramu midzi makumi awiri m'dziko la Galileya.