1 Kings 9:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
(Farao mfumu ya ku Ejipito anali atalanda mzinda wa Gezere, nautentha. Adaapha Akanani amene ankakhala mumzindamo ndipo adaupereka kuti ukhale mphatso kwa mwana wake wamkazi, uja adaakwatiwa ndi Solomoniyu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti Farao mfumu ya Aejipito adakwera nalanda Gezere, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wake mkazi wa Solomoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
(Farao mfumu ya ku Igupto inali itathira nkhondo ndi kulanda Gezeri. Iye anatentha mzindawo. Anapha Akanaani amene ankakhala mʼmenemo ndipo kenaka anawupereka ngati mphatso yaukwati kwa mwana wake wamkazi amene anakwatiwa ndi Solomoni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti Farao mfumu ya Aigupto adakwera nalanda Gezeri, nautentha ndi moto, nawapha Akanani akukhala m'mudzimo, naupereka kwaulere kwa mwana wace mkazi wa Solomo.